Ezekiel 16:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe sudakhutire nkutsata njira zao zoipa ndiponso kuchita zonyansa. Koma patangopita nthaŵi pang'ono chabe, unkachita zoipa kupambana iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sunayenda m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe sunangotsatira kokha njira zawo zoyipa ndi kuchita zonyansa zawo, koma patangopita nthawi pangʼono machitidwe ako oyipa anaposa awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sunayenda m'njira zao, kapena kucita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kubvunda kwako, m'njira zako zonse.