Ezekiel 16:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tchimo la mbale wako Sodomu linali lakuti iyeyo pamodzi ndi midzi yake ankanyadira chuma chake ndi chakudya chake chambiri, koma osalabadako zothandiza osauka ndi aumphaŵi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, mphulupulu ya mng'onowako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kucuruka kwa cakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ace; ndipo sanalimbitsa dzanja la wosauka ndi wosowa.