Ezekiel 16:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adakusamala kapena kukumvera chisoni chokwanira kuti akuchitire zimenezi. Koma adakutaya panja poyera, chifukwa adaanyansidwa nawe pa tsiku limene udabadwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Panalibe diso linakuchitira chifundo, kukuchitira chimodzi chonse cha izi, kuchitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibe ndi mmodzi yemwe anakusamala kapena kukumvera chisoni kuti akuchitire zimenezi. Mʼmalo mwake anakutaya panja poyera, chifukwa ananyansidwa nawe pa tsiku lako lobadwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Panalibe diso linakucitira cifundo, kukucitira cimodzi conse ca izi, kucitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwake,