Ezekiel 16:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale Samariya yemwe sadachite theka la machimo amene udachita iwe. Iweyo udachita zonyansa zambiri kupambana abale ako aŵiriwo, kotero kuti iwo amaoneka ngati osachimwa poyerekeza ndi iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngakhale Samariya sanachite theka la zochimwa zako, koma unachulukitsa zonyansa zako, kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samariya sanachite ngakhale theka la machimo amene unachita. Iwe wachita zinthu zonyansa zambiri kuposa iwo, motero kuti abale ako awiriwo amaoneka ngati olungama kuyerekeza ndi iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngakhale Samariya sanacita theka la zocimwa zako, koma unacurukitsa zonyansa zako kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazicita.