Ezekiel 16:52 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano mwiniwakewe uyenera kuchita manyazi ndi kunyozedwa, iwe amene waonetsa abale ako ngati osachimwa. Machimo ako ndi onyansa kwambiri kupitirira a abale ako, motero iwo aoneka ngati osalakwa. Iwenso tsono, amene udaonetsa abale ako ngati osachimwa, uchite manyazi ndi kunyozedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zochimwa zako unazichita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m'chilungamo chao, nawenso uchite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iwenso uyenera kuchita manyazi popeza waonetsa abale ako ngati osachimwa. Popeza kuti machimo ako ndi onyansa kwambiri kupambana awo, tsonotu iwowo akuoneka olungama kupambana iweyo. Choncho iwenso uchite manyazi ndi kunyozedwa popeza unaonetsa abale ako ngati olungama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zocimwa zako unazicita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m'cilungamo cao, nawenso ucite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama.