Ezekiel 16:55 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene mbale wako Sodomu pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, ndipo pamene mbale wako Samariya pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, nawenso ndi midzi yako udzakhalanso monga momwe udaaliri kale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ake adzabwerera umo unakhalira kale, ndipo Samariya ndi ana ake adzabwerera umo anakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero mʼbale wako Sodomu ndi ana ake akadzakhala monga mmene analili poyamba paja, ndiponso mʼbale wako Samariya akadzakhalanso monga mmene anali poyamba paja, ndiye kuti iwenso ndi ana ako mudzakhala monga mmene munalili payamba paja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ace adzabwerera umo unakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale.