Ezekiel 16:57 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuipa kwako kusanadziŵike. Koma tsopano walingana naye posanduka chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse oyandikana nawo, ndiponso kwa Afilisti. Ndithu okuzungulira onsewo akukunyoza kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chisanavundukuke choipa chako monga nthawi ya chitonzo cha ana akazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana akazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuyipa kwako kusanadziwike? Koma tsopano wafanana naye. Wasandukano chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse owazungulira ndiponso kwa Afilisti. Ndithu onse amene akuzungulira amakunyoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cisanabvundukuke coipa cako monga nthawi ya citonzo ca ana akazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana akazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.