Ezekiel 16:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Ndiye Ine nditabwera, ndidakuwona ukuvimvinizika m'magazi ako. Ndidalankhula nawe uli m'magazi momwemo ndi kukuuza kuti, “Ukhale ndi moyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikuvimvinizika m'mwazi mwako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako. Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Tsono pamene ndinkadutsa, ndinakuona ukuvimvinizika mʼmagazi ako. Ndinakuyankhula uli mʼmagazi ako omwewo kuti, ‘Khala ndi moyo,’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikubvimvinizika m'mwazi wako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako, Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.