Ezekiel 16:61 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono udzakumbukira makhalidwe ako akale. Udzachita manyazi pamene udzalandiranso abale ako, wamkulu ndi wamng'ono yemwe. Ndidzaŵapereka kwa iwe kuti akhale ngati ana ako aakazi, ngakhale kuti iwowo sali nao m'chipangano changa ndi iwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo udzakumbukira njira zako ndi kuchita manyazi, pakulandira abale ako akulu ndi ang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako akazi, angakhale sali a pangano lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono udzakumbukira njira zako zakale. Udzachita manyazi polandiranso abale ako, wamkulu ndi wamngʼono yemwe. Ndidzawaperekanso kwa iwe kuti akhale ngati ana ako ngakhale kuti sali a mʼpangano langa ndi iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo udzakumbukila njira zako ndi kucita manyazi, pakulandira abale ako akuru ndi ang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako akazi, angakhale sali a pangano lako.