Ezekiel 16:63 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikadzakukhululukira zoipa zako zonse zimene udachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzathanso nkulankhula komwe. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikadzakukhululukira zoyipa zako zonse zimene unachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzatha nʼkuyankhula komwe, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti uzikumbukila ndi kucita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, cifukwa ca manyazi ako, pamene ndikufafanima zonse unazicita, ati Ambuye Yehova.