Ezekiel 16:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Nditabweranso, ndidaona kuti nthaŵi yako yomanga banja idakwana. Tsono ndidakufunditsa mwinjiro wanga ndi kubisa maliseche ako. Ndidachita nawe chipangano chaukwati, ndipo udasanduka wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Tsono pamene ndinkadutsanso ndinaona kuti nthawi yako yomanga banja inakwana. Tsono ndinakufunditsa chovala changa ndi kubisa umaliseche wako. Ndinachita nawe pangano la ukwati ndipo unakhala wanga, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakupfunda copfunda canga, ndi kuphimba umarisece wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.