Ezekiel 17:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uŵafunse anthu aupanduŵa kuti, ‘Kodi mukulidziŵa tanthauzo lake la zimenezi?’ Uŵauze kuti mfumu ya ku Babiloni idaapita ku Yerusalemu, nikatengako mfumu ndi akalonga ake kupita nawo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uziti, tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nchiyani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babiloni inadza ku Yerusalemu, nitenga mfumu yake ndi akalonga ake, nibwera nao kuli iye ku Babiloni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tawafunsa anthu owukirawa kuti, ‘kodi mukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Uwafotokozere kuti, ‘Mfumu ya Babuloni inapita ku Yerusalemu ndikukatengako mfumu ndi anthu ake otchuka ndi kubwera nawo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uziti tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nciani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babulo inadza ku Yerusalemu, nitenga mfumu yace ndi akalonga ace, nibwera nao kuti iye ku Babulo;