Ezekiel 17:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mfumuyo idapandukira mfumu ya ku Babiloni, nitumiza akazembe ku Ejipito kukapempha akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. Kodi mfumu yoteroyo ingapambane? Kodi ingathe kupulumuka ngati ichita zotero? Kodi ingathe kuphwanya chipangano, kenaka nkupulumuka?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mfumu inawukira mfumu ya ku Babuloni potumiza nthumwi ku dziko la Igupto kukatenga akavalo ndi gulu lalikulu la nkhondo. Kodi mfumu yotereyi ingapambane? Kodi wochita zinthu zoterezi angapulumuke? Kodi angaphwanye mgwirizano ndi kupulumuka?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yace ku Aigupto, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? adzapulumuka wakucita izi? atyole pangano ndi kupulumuka kodi?