Ezekiel 17:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikulumbira pali Ine ndemwe wamoyo, kuti mfumuyo idzafera ku Babiloni, dziko lomwe la mfumu imene idamulonga ufumuyo. Idapeputsa lumbiro lake, nkuphwanya chipangano chimene idachita ndi mfumu inayo. Motero idzafera ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamchititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lake, imene anathyola pangano lake, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, mfumuyo idzafera ku Babuloni, mʼdziko la mfumu imene inayika pa mpando waufumu. Inapeputsa lumbiro lake nʼkuphwanya pangano limene inachita ndi mfumu inayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamcititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lace, imene anatyola pangano lace, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babulo.