Ezekiel 17:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali Ine ndemwe wamoyo, iyeyo wapeputsa lumbiro lake limene adalumbira kwa Ine, ndipo waphwanya chipangano chimene ndidapangana naye. Motero ndidzamlanga chifukwa cha zoipa zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analithyola, ndidzawabweza pamutu pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndithu pali Ine wamoyo, Ine ndidzalanga mfumu imeneyi chifukwa inanyoza lumbiro langa, ndi kuphwanya pangano langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analityola, ndidzawabweza pamutu pace.