Ezekiel 17:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzamtchera ukonde, ndipo ndidzamkola mu msampha wanga. Ndidzamtengera ku Babiloni, ndipo ndidzamlangira komweko, chifukwa choti sadakhulupirike kwa Ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babiloni, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwake anandilakwira nako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzayitchera ukonde ndipo idzakodwa mu msampha wanga. Ndidzapita nayo ku Babuloni ndi kuyilanga kumeneko chifukwa inali yosakhulupirika kwa Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babulo, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwace anandilakwira nako.