Ezekiel 17:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asilikali ake onse amphamvu adzaphedwa ku nkhondo, ndipo opulumuka adzathaŵira ku mbali zonse. Motero mudzadziŵa kuti ndine Chauta amene ndanena zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo othawa ake onse m'magulu ake onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa kumphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asilikali ake onse amene akuthawa adzaphedwa ndi lupanga, ndipo opulumuka adzabalalitsidwa ku mbali zonse. Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova ndayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo othawa ace onse m'magulu ace onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa ku mphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.