Ezekiel 17:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “Ine ndemwe ndidzatenga kanthambi ka ku nsonga yapamwamba ya mtengo wa mkungudza, ndipo ndidzakabzala. Pa tinthambi tapamwamba ndidzathyolako kena kanthete ndipo ndidzakabzala pa phiri lalitali kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kuiika; ndidzabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kuioka pa phiri lalitali lothuvuka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndidzatenga nthambi pamwamba penipeni pa mkungudza ndi kuyidzala; ndidzathyola nthambi yanthete kuchokera pa nthambi zapamwamba penipeni ndi kuyidzala pamwamba pa phiri lalitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kulika; ndidzabudula nsonga yosomphoka'ya nthambi zace zanthete, ndi kuioka pa phiri lalitali lothubvuka;