Ezekiel 17:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakabzaladi pa phiri lalitali la ku Israele. Kadzaphuka ndi kubala zipatso zake. Motero kadzasanduka mkungudza wokoma. Mbalame za mitundu yonse zidzakhala mu mthunzi wa mtengowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pa phiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko ali onse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzayidzaladi pa phiri lalitali la Israeli. Idzaphuka nthambi ndi kubereka zipatso. Choncho idzasanduka mkungudza wamphamvu. Mbalame za mtundu uliwonse zidzamanga zisa zawo mʼmenemo; zidzapeza malo okhala mu mthunzi wa nthambi zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pa phiri lothubvuka la Israyeli ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwace mudzakhala mbalame ziri zonse za mapiko ali onse; mu mthunzi wa nthambi zace zidzabindikira.