Ezekiel 17:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitengo yonse yam'dzikomo idzadziŵa kuti ndine Chautane amene ndimafupikitsa mitengo yaitali, ndiponso kutalikitsa mitengo yaifupi. Ndimaumitsa mitengo yobiriŵira, ndi kubiriŵiritsa mitengo youma. Ine Chauta ndanena zimenezi, ndipo ndidzazichitadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mitengo yonse ya kuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kuchichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine ndine Yehova amene ndimafupikitsa mitengo yayitali ndi kutalikitsa mitengo yayifupi. Ndimawumitsa mitengo yabiriwiri ndi kubiriwitsa mitengo yowuma. “ ‘Ine Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichita.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mitengo yonse ya kuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kucicita.