Ezekiel 17:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Unene kuti Ambuye Chauta akuti, Panali chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko akuluakulu, ndi nthenga zitalizitali za mathothomathotho. Chidadza ku Lebanoni. Chidagwira nthambi yapamwamba pa mtengo wa mkungudza,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuziti, Atero Ambuye Yehova, Chiombankhanga chachikulu ndi mapiko akulu, ndi maphiphi atali, odzala nthenga cha mathothomathotho, chinafika ku Lebanoni, nichitenga nsonga ya mkungudza,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwawuze kuti Ambuye Yehova akuti, chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko amphamvu, nthenga zitalizitali zamathothomathotho chinabwera ku Lebanoni. Chinagwira nthambi ya pamwamba pa mtengo wa mkungudza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ciombankhanga cacikuru ndi mapiko akuru, ndi maphiphi atali, odzala nthenga ca mathotho-mathotho, cinafika ku Lebano, nicitenga nsonga ya mkungudza,