Ezekiel 17:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono idaphuka nisanduka mtengo wamphesa wotambalala cham'munsi. Nthambi zake zidaloza kumwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake idazamira pansi. Choncho mtengo wamphesawo udasanduka wanthambi ndi wa masamba ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala waufupi msinkhu, nthambi zake zinapindikira momwe, ndi mizu yake pansi pake, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inaphuka nisanduka mtengo wa mpesa wotambalala chamʼmunsi. Nthambi zake zinaloza mmwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake inalowa pansi. Kotero unakhala mtengo wamphesa ndipo unasanduka wa nthambi ndiponso wa masamba ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala wofupi msinkhu, nthambi zace zinapindikira momwe, ndi mizu yace pansi pace, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.