Ezekiel 17:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu cha mapiko akuluakulu ndi cha nthenga zambiri. Mtengo wamphesa uja udapinda mizu yake kulozetsa kwa chiwombankhangacho. Ndipo udayang'anitsa nthambi zake kwa chimbalamecho, kuti mwina nkuzithirira madzi oposa amene anali m'mundamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Panalinso chiombankhanga china chachikulu, ndi mapiko akulu, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unachipindira mizu yake, nuchilunjikitsira nthambi zake, kuchokera pookedwa pake, kuti chiuthirire madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu, cha mapiko amphamvu ndi cha nthenga zambiri. Tsopano mtengo wamphesa uja unakhotetsera mizu yake kwa chiwombankhangacho kuchokera pa malo amene unadzalidwa ndipo unatambalitsa nthambi zake kwa chiwombankhangacho kufuna kuthiridwa madzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Panalinso ciombankhanga cina cacikuru, ndi mapiko akuru, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unacipindira mizu yace, nucilunjikitsira nthambi zace, kucokera pookedwa pace, kuti ciuthirire madzi.