Ezekiel 17:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ukanene kuti, Ambuye Chauta akuti, Kodi mtengo wamphesa umenewu udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzauzula mizu ndi kubudula nthambi zake, kotero kuti masamba ake anthete adzafota? Nkosalira munthu wamphamvu kapena anthu ochuluka kuti auzuletu ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? Sadzausula ndi kudula zipatso zake, kuti uume, kuti masamba ake onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikulu, kapena anthu ambiri akuuzula?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ukawawuze Aisraeli kuti, ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Kodi udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzawuzula mizu ndi kubudula nthambi zake kuti ufote? Masamba ake onse anthete adzafota. Sipadzafunika dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti awuzule.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? sadzausula ndi kudula zipatso zace, kuti uume, kuti masamba ace onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikuru, kapena anthu ambiri akuuzula?