Ezekiel 18:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwina mwake munthu woipa uja nkubala mwana amene aona machimo a bambo wake. Amaona, koma satsanzirako. Sadyera nao ku zitunda zachipembedzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zochimwa zonse adazichita atate wake, naopa wosachita zoterezo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zocimwa zonse adazicita atate wace, naopa wosacita zoterezo,