Ezekiel 18:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
sazunza munthu wina aliyense, satenga chigwiriro ndipo saaba. Koma amadyetsa anjala ndi kuveka ausiŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena kusautsa wina aliyense, wosatenga chigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sapondereza munthu wina aliyense. Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka. Salanda zinthu za munthu. Amapereka chakudya kwa anthu anjala. Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena kusautsa wina ali yense, wosatenga cigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,