Ezekiel 18:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amakana kuchita zoipa, sakongoza kuti apezepo phindu kapena kuti alandire chiwongoladzanja. Amatsata malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu woteroyo sadzafera zolakwa za bambo wake. Adzakhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
naletsa dzanja lake pa wozunzika, wosalandira phindu kapena choonjezerapo, wochita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wake, adzakhala ndi moyo ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amadziletsa kuchita zoyipa. Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja. Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naletsa dzanja lace pa wozunzika, wosalandira phindu kapena coonjezerapo, wocita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wace, adzakhala ndi moyo ndithu.