Ezekiel 18:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwina mungathe kufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha zolakwa za bambo wake?’ Mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa choti nthaŵi zonse ankachita zolungama ndi zokhulupirika, ndipo ankamvera malamulo anga onse mosamala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wake? Mwanayo akachita chiweruzo ndi chilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwachita, adzakhala ndi moyo ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wace? Mwanayo akacita ciweruzo ndi cilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwacita, adzakhala ndi moyo ndithu.