Ezekiel 18:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wochimwa ndiye amene adzafe, osati wina. Mwana sadzafera machimo a bambo wake, ndipo bambo sadzafera machimo a mwana wake. Munthu wabwino adzakolola zipatso za ubwino wake. Munthu woipa adzakolola zipatso za kuipa kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Moyo wochimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; chilungamo cha wolungama chidzamkhalira, ndi choipa cha woipa chidzamkhalira,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Moyo wocimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu zaatate wace, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; cilungamo ca wolungama cidzamkhalira, ndi coipa ca woipa cidzamkhalira,