Ezekiel 18:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu wochimwa akaleka machimo ake amene ankachita, namamvera malamulo anga onse, ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndithudi ameneyo adzakhala ndi moyo, sadzafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma woipayo akabwerera kusiya machimo ake onse adawachita nakasunga malemba anga onse, ndi kuchita chiweruzo ndi chilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma woipayo akabwerera kusiya macimo ace onse adawacita nakasunga malemba anga onse, ndi kucita ciweruzo ndi cilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.