Ezekiel 18:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi imfa ya munthu woipa Ine ndimakondwera nayo? Iyai, koma ndikadakonda kuti woipa aleke njira zake zoipa ndi kukhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yace, ndi kukhala ndi moyo?