Ezekiel 18:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma munthu wabwino akasanduka woipa, namachita zonyansa za mitundu yonse zimene anthu amachita, kodi munthu woteroyo nkukhala ndi moyo? Iyai, ntchito zake zonse zabwino sizidzakumbukika. Wapalamula, wachimwa, adzafa basi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m'kulakwa kwake analakwa nako, ndi m'kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma wolungamayo akabwerera kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, ndi kucita monga mwa zonyansa zonse azicita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena cimodzi ca zolungama zace zonse adzazicita cidzakumbukika m'kulakwa kwace analakwa nako, ndi m'kucimwa kwace anacimwa nako; momwemo adzafa.