Ezekiel 18:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu mumati, ‘A! Zimene Ambuye amachitazi nzopanda chilungamo.’ Tamvani tsono Aisraele inu: Kani zochita zanga ndiye zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene zili zosalungama?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israele, Kodi njira yanga njosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israyeli, Kodi njira yanga njosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?