Ezekiel 18:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati munthu wabwino aleka kuchita zoyenera, namachita zoipa, adzafa chifukwa cha zoipa zakezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolungamayo akatembenukira kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yake adaichita adzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolungamayo akatembenukira kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yace adaicita adzafa.