Ezekiel 18:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tayani, ndi kudzicotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israyeli?