Ezekiel 18:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa mwana ndi wanga, wa bambo ndi wanganso. Munthu amene wachimwa, ndiye amene adzafe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wocimwawo ndiwo udzafa.