Ezekiel 18:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo sadyera nao ku zitunda zachipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israele. Saipitsa mkazi wa munthu wina. Sakhudza mkazi pamene ali wosamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
wosadya pamapiripo, wosakweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo kapena kupembedza mafano a Aisraeli. Iye sayipitsa mkazi wa mnzake kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
wosadya pamapiripo, wosakweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,