Ezekiel 18:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sazunza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole chigwiriro chake. Saaba, amadyetsa anjala, ndipo amaveka ausiwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sapondereza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake. Iye salanda zinthu za osauka, koma amapereka chakudya kwa anthu anjala, ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
wosasautsa munthu ali yense, koma wambwezera wangongole cigwiriro cace, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,