Ezekiel 19:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Unali ndi nthambi zolimba zoyenera kupangira ndodo zaufumu. Udatalika nusomphoka pakati pa zomera zina, ndipo unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake ndi kuchuluka kwa nthambi zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zachifumu, za ochita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, nizinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zake zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthambi zake zinali zolimba, zoyenera kupangira ndodo yaufumu. Unatalika nusomphoka pakati pa zomera zina. Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake, ndi nthambi zake zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zacifumu, za ocita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, nizinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zace zambiri.