Ezekiel 19:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Mai wako anali ngati mkango waukazi pakati pa mikango yaimuna. Ankagona pakati pa mikango yaimuna akulera ana ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
uziti, Mai wako ndi chiyani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ake pakati pa misona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uzinena kuti, “ ‘Amayi ako anali ndani? Anali ngati mkango waukazi! Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna; unkalera ana ake pakati pa misona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
uziti, Mai wako ndi ciani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ace pakati pa misona.