Ezekiel 19:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mitundu ya anthu idachenjezana za mkangowo, ndipo tsiku lina udagwa m'mbuna yao. Adaukoka ndi ngoŵe kupita nawo ku dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mitundu ya anthu idamva mbiri yake, unagwidwa m'mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera kudziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amitundu anamva za mkangowo, ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo. Iwo anawukoka ndi ngowe kupita nawo ku dziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mitundu ya anthu idamva mbiri yace, unagwidwa m'mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera ku dziko la Aigupto.