Ezekiel 19:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udagwetsa malinga ao, ndipo udaononga mizinda yao. Onse a m'dzikolo adachita mantha chifukwa cha phokoso la kubangula kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula midzi yao, ndipo dziko ndi kudzala kwake linasanduka labwinja, chifukwa cha phokoso la kubangula kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Unagwetsa malinga awo, ndikuwononga mizinda yawo. Onse a mʼdzikomo anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula midzi yao, ndipo dziko ndi kudzala kwace linasanduka labwinja, cifukwa ca phokoso la kubangula kwace.