Ezekiel 19:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaukoka ndi ngoŵe nauponya m'chitatanga. Adapita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni, mfumuyo nkuuponya m'ndende. Choncho liwu lake silidamvekenso ku mapiri a ku Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nauika m'chitatanga ndi zokowera, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni; anaulonga m'malinga, kuti mau ake asamvekenso pa mapiri a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga. Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso ku mapiri a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nauika m'citatanga ndi zokowera, nadza nao kwa mfumu ya ku Babulo; anaulonga m'malinga, kuti mau ace asamvekenso pa mapiri a Israyeli.