Ezekiel 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukutuma kwa Israele, mtundu wa anthu aupandu amene andipandukira. Iwowo ndi makolo ao akhala akundichimwira mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israele, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikukutuma kwa Aisraeli, mtundu wa anthu owukira umene wandiwukira Ine; Iwo ndi makolo awo akhala akundiwukira Ine mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israyeli, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe.