Ezekiel 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha ndipo usaope zimene azikanena. Usachite mantha ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Komabe usaope mau ao ndipo usade nkhaŵa ndi mapenyedwe ao, chifukwa anthuwo ngaupandu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika