Ezekiel 2:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma tsono iwe mwana wa munthu, umvere bwino zimene ndikukuuza. Usakhale waupandu ngati iwowo. Tsopano yasama, udye chimene ndikupatse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ichi ndilikunena nawe; usakhale iwe wopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye chomwe ndikupatsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuwuza. Usakhale wowukira ngati iwowo. Tsono yasama pakamwa pako kuti udye chimene ndikukupatsa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ici ndirikunena nawe; usakhale iwewopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye comwe ndikupatsa.