Ezekiel 20:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ukapolo, akuluakulu ena a ku Israele adabwera kudzapempha nzeru kwa Chauta. Tsono adakhala pansi pamaso panga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chiwiri, mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israele kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiwiri, ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kudzapempha nzeru kwa Yehova, ndipo anakhala pansi pamaso panga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali caka cacisanu ndi ciwiri, mwezi wacisanu; tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israyeli kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga.