Ezekiel 20:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaŵapatsanso masiku a Sabata kuti akhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziŵe kuti Ine Chauta ndimaŵayeretsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawapatsanso Masabata ngati chizindikiro pakati pathu, kuti adziwe kuti Ine Yehova ndinawapatula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale cizindikilo pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.