Ezekiel 20:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Aisraele adandipandukira m'chipululumo. Sadatsate malangizo anga ndipo adakana malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Anthuwo adaipitsa kotheratu masiku anga a Sabata. Motero Ine ndidaganiza zoŵalanga mwaukali m'chipululu momwemo ndi kuŵaononga kotheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Komabe anthu a Israeli anandiwukira mʼchipululu. Iwo sanatsatire malangizo anga koma anakana malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndipo anayipitsa kotheratu Masabata anga. Choncho, ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawononga mʼchipululu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nyumba ya Israyeli inapaodukira Ine m'cipululu, sanayenda m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene, munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'cipululu kuwatha.