Ezekiel 20:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma zimenezo sindidazichite, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene adandiwona ndikutulutsa Aisraelewo ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawaturutsa pamaso pao.